5 Ndipo anati kwa iye mnyamatayo, Kapena sadzafuna mkaziyo kunditsata ine ku dziko lino: kodi ndikambwezerenso mwana wanu kudziko komwe mwacokera inu?
6 Ndipo Abrahamu anati kwa iye, Cenjera iwe, usambwezerenso mwana wanga kumeneko.
7 Yehova Mulungu wa Kumwamba, amene ananditenga ine ku nyumba ya atate wanga, ku dziko la abale anga, amene ananena ndi ine, amene analumbirira ine kuti, Ndidzapatsa mbeu zako dziko ili; iye adzatumiza mthenga wace akutsogolere, ndipo udzamtengere mwana wanga mkazi kumeneko.
8 Ndipo ngati sadzafuna mkaziyo kukutsata iwe, udzakhala wosacimwa pa cilumbiro cangaci: koma mwana wanga usambwezerenso kumeneko.
9 Ndipo mnyamatayo anaika dzanja lace pansi pa ncafu yace ya Abrahamu mbuye wace, namlumbirira iye za cinthuco.
10 Ndipo mnyamatayo anatenga ngamila khumi za mbuyace, namuka: cifukwa kuti cuma conse ca mbuyace cinali m'dzanja lace: ndipo anacoka namuka ku Mesopotamiya, ku mudzi wa Nahori.
11 Ndipo anagwaditsa ngamila zace kunja kwa mudzi, ku citsime ca madzi nthawi yamadzulo, nthawi yoturuka akazi kudzatunga madzi.