6 Ndipo Abrahamu anati kwa iye, Cenjera iwe, usambwezerenso mwana wanga kumeneko.
7 Yehova Mulungu wa Kumwamba, amene ananditenga ine ku nyumba ya atate wanga, ku dziko la abale anga, amene ananena ndi ine, amene analumbirira ine kuti, Ndidzapatsa mbeu zako dziko ili; iye adzatumiza mthenga wace akutsogolere, ndipo udzamtengere mwana wanga mkazi kumeneko.
8 Ndipo ngati sadzafuna mkaziyo kukutsata iwe, udzakhala wosacimwa pa cilumbiro cangaci: koma mwana wanga usambwezerenso kumeneko.
9 Ndipo mnyamatayo anaika dzanja lace pansi pa ncafu yace ya Abrahamu mbuye wace, namlumbirira iye za cinthuco.
10 Ndipo mnyamatayo anatenga ngamila khumi za mbuyace, namuka: cifukwa kuti cuma conse ca mbuyace cinali m'dzanja lace: ndipo anacoka namuka ku Mesopotamiya, ku mudzi wa Nahori.
11 Ndipo anagwaditsa ngamila zace kunja kwa mudzi, ku citsime ca madzi nthawi yamadzulo, nthawi yoturuka akazi kudzatunga madzi.
12 Ndipo anati, Yehova, Mulungu wa mbuyanga Abrahamu mundiyendetse ine bwino lero lino, mumcitire ufulu mbuyanga Abrahamu,