11 Yakobo ndipo anati kwa Rebeka amace, Taonani, Esau mkuru wanga ndiye munthu waubweya, ine ndine munthu, wosalala.
12 Kapena atate wanga adzandiyambasa, ndipo ndidzaoneka pamaso pace ngati wakunyenga; pamenepo ndidzadzitengera ine temberero, si mdalitso.
13 Ndipo amace anati kwa iye, Pa ine likhale temberero lako mwana wanga; koma tamvera mau anga, kazimuka kunditengera timeneto.
14 Ndipo anamuka nakatenga nadza nato kwa amace; amace ndipo anakonza cakudya cokolera conga cimene anacikonda atate wace.
15 Ndipo Rebeka anatenga zobvala zokoma za Esau, mwana wace wamkuru zinali m'nyumba, nabveka nazo Yakobo mwana wace wamng'ono;
16 ndipo anabveka zikopa za tiana tambuzi pa manja ace ndi pakhosi pace posalala;
17 ndipo anapereka m'dzanja la mwana wace Yakobo cakudya cokoleraco, ndi mikate imene anaipanga.