15 Ndipo Rebeka anatenga zobvala zokoma za Esau, mwana wace wamkuru zinali m'nyumba, nabveka nazo Yakobo mwana wace wamng'ono;
16 ndipo anabveka zikopa za tiana tambuzi pa manja ace ndi pakhosi pace posalala;
17 ndipo anapereka m'dzanja la mwana wace Yakobo cakudya cokoleraco, ndi mikate imene anaipanga.
18 Ndipo iye analowa kwa atate wace, nati, Atate wanga; iye anati, Ndine pano; ndani iwe mwana wanga?
19 Ndipo Yakobo anati kwa atate wace, Ndine Esau mwana wanu wamkuru; ndacita monga mwandiuza ine; ukanitu, khalani tsonga, idyani nyama yanga kuti moyo wanu undidalitse ine.
20 Ndipo Isake anati kwa mwana wace, Unaipeza msanga bwanji mwana wanga? Ndipo anati, Cifukwa kuti Yehova Mulungu wanu anandiyendetsa ine bwino.
21 Ndipo Isake anati kwa Yakobo, Sendera kuno, ndikuyambase mwana wanga, ngati ndiwe mwana wanga Esau ndithu, kapena wina.