30 mfumu Disoni, mfumu Ezeri, mfumu Disani; amenewa ndi mafumu obadwa kwa Ahori, monga mwa maufumu ao m'dziko la Seiri.
31 Amenewo ndi mafumu analamulira m'dziko la Edomu, asadalamulire ana a Israyeli mfumu ali yense.
32 Ndipo Bela mwana wamwamuna wa Beori, analamulira m'Edomu, ndipo dzina la mudzi wace ndilo Dinaba.
33 Ndipo Bela anamwalira, ndipo Jobabi mwana wamwamuna wa Zera wa ku Bozara analamulira m'malomwace.
34 Ndipo Jobabi anamwalira, ndipo Husami wa ku dziko la Atemani analamulira m'malo mwaceo
35 Ndipo Husami anamwalira, ndipo Hadadi mwana wamwamuna wa Bedadi, amene anakantha Midyani m'dambo la Moabu, analamulira m'malo mwace: dzina la mudzi wace ndi Avita.
36 Ndipo Hadadi anamwalira, ndipo Samila wa ku Masereka analamulira m'malo mwace.