1 Ndipo Yosefe anauza tsanyumba wace kuti, Dzaza matumba a anthuwo ndi cakudya, monga angathe kunyamula, ndi kuika ndalama za yense kukamwa kwa thumba lace.
2 Nuike cikho canga, cikho casiliva ciija, kukamwa kwa thumba la wamng'ono, pamodzi ndi ndalama za tirigu zace. Ndipo iye anacita monga mau ananena Yosefe.
3 Pamene kudaca, anamukitsa anthu iwo ndi aburu ao.
4 Ataturuka m'mudzi asanamuke patari, Yosefe anati kwa tsanyumba wace, Tanyamuka, talondola anthu aja, ukawapeza unene nao, Cifukwa canji mwabwezera zoipa m'malo mwa zabwino?
5 Kodi si ndico comwera naco mbuyanga, naombeza ula naco? Mwacitira coipa pakutero.