18 Ndipo Yosefe anati kwa atate wace, Msatero atate wanga, cifukwa uyu ndi woyamba; ikani dzanja lanu lamanja pa mutu wace.
19 Koma anakana atate wace, nati, Ndidziwa mwananga, ndidziwa; Iyenso adzakhala mtundu wa anthu, iyenso adzakula; koma mphwace adzakhala wamkuru ndi iye, ndipo mbeu zace zidzakhala mitundu yambirimbiri.
20 Ndipo anadalitsa iwo tsiku lomwelo, nati, Mwa iwe Israyeli adzadalitsa, kuti, Mulungu akuyese iwe monga Efraimu ndi monga Manase; ndipo anaika Efraimu woyamba wa Manase.
21 Ndipo Israyeli anati kwa Yosefe, Taona, ndirinkufa ine; Mulungu adzakhala ndi iwe, adzakubwezanso iwe ku dziko la makolo ako.
22 Ndipo ine ndakupatsa iwe gawo limodzi loposa la abale ako, limene ndinalanda m'dzanja la Aamori ndi lupanga langa ndi uta wanga.