28 Awa onse ndiwo mafuko khumi ndi awiri a Israyeli: izo ndizo zomwe ananena kwa iwo atate wao nawadalitsa; yense monga mdalitso wace anawadalitsa.
29 Ndipo analangiza iwo nati kwa iwo, Ine nditi ndisonkhanizidwe kwa anthu a mtundu wanga; mundiike ine pamodzi ndi makolo anga m'phanga liri m'munda wa Efroni Mhiti,
30 m'phanga liri m'munda wa Makipela, umene uli patsogolo pa Mamre, m'dziko la Kanani, limene Abrahamu analigula kwa Efroni Mhiti pamodzi ndi munda, likhale poikira pace:
31 pamenepo anaika Abrahamu ndi Sara mkazi wace; pamenepo anaika Isake ndi Rebeka mkazi wace: pamenepo ndinaika Leya:
32 munda ndi phanga liri m'menemo, zinagulidwa kwa ana a Heti.
33 Pamene Yakobo anatha kulangiza ana ace amuna, anafunya mapazi ace pakama, natsirizika, nasonkhanizidwa kwa anthu a mtundu wace.