6 Masiku onse akudzipatulira kwa Yehova asayandikize mtembo.
7 Asadzidetse ndi atate wace, kapena mai wace, mbale wace, kapena mlongo wace, akafa iwowa; popeza cowindira Mulungu wace ciri pamutu pace.
8 Masiku onse a kusala kwace akhala wopatulikira kwa Yehova.
9 Munthu akafa cikomo pali iye, ndipo akadetsa mutu wace wowinda; pamenepo azimeta mutu wace tsiku la kumyeretsa kwace, tsiku lacisanu ndi ciwiri aumete.
10 Ndipo tsiku lacisanu ndi citato adze nazo njiwa ziwiri, kapena maunda awiri, kwa wansembe, ku khomo la cihema cokomanako;
11 ndipo wansembe akonze imodzi nsembe yaucimo, ndi yina nsembe yopsereza, namtetezere popeza anacimwa nao mtembowo; ndipo apatulire mutu wace tsiku lomwelo.
12 Ndipo awapatulire Yehova masiku a kusala kwace, nadze nayo nkhosa yamphongo ya caka cimodzi ikhale nsembe yoparamula; koma masiku adapitawa azikhala cabe, popeza anadetsa kusala kwace.