10 Mafaniziro a nkhope zao zinali nayo nkhope ya munthu; ndi izi zinai zinali nayo nkhope ya mkango pa mbali ya ku dzanja lamanja; ndi izi zinai zinali nayo nkhope ya ng'ombe pa mbali ya ku dzanja lamanzere; izi zinai zinali nayonso nkhope ya ciombankhanga.
11 Ndi nkhope zao ndi mapiko ao zinagawikana kumutu; ciri conse cinali nao mapiko awiri olumikizana, ndi awiri anaphimba thupi.
12 Ndipo zinayenda, ciri conse cinalunjika kutsogolo kwace uko mzimu unafuna kumukako zinamuka, sizinatembenuka poyenda.
13 Kunena za mafaniziro a zamoyozo, maonekedwe ao ananga makara amoto, monga maonekedwe a miyuni; motowo unayendayenda pakati pa zamoyozo, ndi motowo unacita ceza, ndi m'motomo mudaturuka mphezi.
14 Ndipo zamoyozo zinathamanga ndi kubwerera, ngati maonekedwe a mphezi yong'anima.
15 Ndipo pakupenyerera ine zamoyozo, taonani, njinga imodzi imodzi yoponda pansi pafupi ndi zamoyozo pa nkhope zao zinai.
16 Maonekedwe a njingazi ndi mapangidwe ao ananga mawalidwe a berulo; ndi izi zinai zinafanana mafaniziro ao; ndi maonekedwe ao ndi mapangidwe ao anali ngati njinga ziwiri zopingasitsana.