13 Kunena za mafaniziro a zamoyozo, maonekedwe ao ananga makara amoto, monga maonekedwe a miyuni; motowo unayendayenda pakati pa zamoyozo, ndi motowo unacita ceza, ndi m'motomo mudaturuka mphezi.
14 Ndipo zamoyozo zinathamanga ndi kubwerera, ngati maonekedwe a mphezi yong'anima.
15 Ndipo pakupenyerera ine zamoyozo, taonani, njinga imodzi imodzi yoponda pansi pafupi ndi zamoyozo pa nkhope zao zinai.
16 Maonekedwe a njingazi ndi mapangidwe ao ananga mawalidwe a berulo; ndi izi zinai zinafanana mafaniziro ao; ndi maonekedwe ao ndi mapangidwe ao anali ngati njinga ziwiri zopingasitsana.
17 Poyenda zinayenda ku mbali zao zinai, zosatembenuka poyenda.
18 Ndi mikombero yace inali yokuzika ndi yoopsa; ndi izi zinai zinali ndi mikombero yao yodzala ndi maso pozungulira pao.
19 Ndipo poyenda zamoyozo, njingazi zinayenda pambali pao; ndipo ponyamuka pansi zamoyozo, njinga zinanyamuka.