5 Ndi m'kati mwace mudaoneka mafaniziro a zamoyo zinai. Ndipo maonekedwe ao ndiwo anafanana ndi munthu,
6 ndi yense anali nazo nkhope zinai, ndi yense wa iwo anali nao mapiko anai.
7 Ndi mapazi ao anali mapazi oongoka, ndi ku mapazi ao kunanga kuphazi kwa mwana wa ng'ombe; ndipo ananyezimira ngati mawalidwe a mkuwa wowalitsidwa.
8 Zinali naonso manja a munthu pansi pa mapiko ao pa mbali zao zinai; ndipo zinaizi zinali nazo nkhope zao ndi mapiko ao.
9 Mapiko ao analumikizana; sizinatembenuka poyenda; ciri conse cinayenda ndi kulunjika kutsogoloko.
10 Mafaniziro a nkhope zao zinali nayo nkhope ya munthu; ndi izi zinai zinali nayo nkhope ya mkango pa mbali ya ku dzanja lamanja; ndi izi zinai zinali nayo nkhope ya ng'ombe pa mbali ya ku dzanja lamanzere; izi zinai zinali nayonso nkhope ya ciombankhanga.
11 Ndi nkhope zao ndi mapiko ao zinagawikana kumutu; ciri conse cinali nao mapiko awiri olumikizana, ndi awiri anaphimba thupi.