1 Pamenepo unandikweza mzimu, nudza nane ku cipata ca kum'mawa ca nyumba ya Yehova coloza kum'mawa; ndipo taonani, pa citseko ca cipata amuna makumi awiri mphambu asanu; ndipo ndinaona pakati pao Yazaniya mwana wa Azuri ndi Pelatiya mwana wa Benaya, akalonga a anthu.
2 Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, awa ndi anthu olingirira za mphulupulu, ndi kupangira uphungu woipa m'mudzi muno;
3 ndiwo akuti, siinafike nyengo yakumanga nyumba; mudzi uwu ndi mphika, ife ndife nyama.
4 Cifukwa cace uwanenere, neneratu, wobadwa ndi munthu iwe.
5 Pamenepo mzimu wa Yehova unandigwera, ndipo ananti kwa ine, Nena, Atero Yehova, Mwatero nyumba ya Israyeli, pakuti ndidziwa zimene zimalowa m'mtima mwanu.
6 Mwacurukitsa ophedwa anu m'mudzi muno, mwadzazanso makwalala ace ndi ophedwawo.
7 Cifukwa cace atero Yehova Mulungu, Ophedwa anu munawaika m'kati mwace, iwo ndiwo nyama imene, ndi mudzi uwu ndiwo mphika; koma inu mudzaturutsidwa m'kati mwace.