4 Cifukwa cace uwanenere, neneratu, wobadwa ndi munthu iwe.
5 Pamenepo mzimu wa Yehova unandigwera, ndipo ananti kwa ine, Nena, Atero Yehova, Mwatero nyumba ya Israyeli, pakuti ndidziwa zimene zimalowa m'mtima mwanu.
6 Mwacurukitsa ophedwa anu m'mudzi muno, mwadzazanso makwalala ace ndi ophedwawo.
7 Cifukwa cace atero Yehova Mulungu, Ophedwa anu munawaika m'kati mwace, iwo ndiwo nyama imene, ndi mudzi uwu ndiwo mphika; koma inu mudzaturutsidwa m'kati mwace.
8 Mwaopa lupanga, tsono ndidzakufikitsirani lupanga, ati Yehova Mulungu.
9 Ndipo ndidzakuturutsani m'kati mwace, ndi kukuperekani m'manja a alendo, ndi kucita maweruzo pakati panu.
10 Mudzagwa ndi lupanga, ndidzakuweruzirani ku malire a Israyeli; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.