2 Wobadwa ndi munthu iwe, Unenere za aneneri a Israyeli onenerawo, nuziti nao onenera za m'mtima mwao mwao, Tamverani mau a Yehova.
3 Atero Ambuye Yehova, Tsoka aneneri opusawo akutsata mzimu wao wao, cinkana sanaona kanthu.
4 Aneneri ako, Israyeli, akhala ngati nkhandwe m'mapululu.
5 Simunakwera kuima mopasuka, kapena kumanganso linga la nyumba ya Israyeli, kuima kunkhondo tsiku la Yehova.
6 Iwo aona zopanda pace, ndi phenda labodza amene anena, Atero Yehova; koma Yehova sanawatuma, nayembekezetsa anthu kuti mauwo adzakhazikika.
7 Simunaona masomphenya opanda pace kodi? simunanena ula wabodza kodi? pakunena inu, Atero Yehova; cinkana sindinanena?
8 Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Popeza mwanena zopanda pace, ndi kuona mabodza, cifukwa cace taonani, ndikhala Ine wotsutsana nanu, ati Ambuye Yehova.