11 kuti nyumba ya Israyeli isasocerenso kusatsata Ine, kapena kudzidetsanso ndi zolakwa zao zonse; koma kuti akhale anthu anga, ndipo ndikhale Ine Mulungu wao, ati Ambuye Yehova.
12 Ndipo anandidzera mau a Yehova akuti,
13 Likandicimwira dziko ndi kucita monyenga, ndipo ndikalitambasulira dzanja langa, ndi kulityolera mcirikizo wace, ndiwo mkate, ndi kulitumizira njala, ndi kulidulira munthu ndi nyama,
14 cinkana akadakhala m'mwemo anthu awa atatu, Nowa, Danieli, ndi Yobu, akadapulumutsa moyo wao wokha mwa cilungamo cao, ati Ambuye Yehova.
15 Ndikapititsa zirombo zoipa pakati pa dziko, nizipulula ana, kuti likhale lacipululu losapitako munthu cifukwa ca zirombo,
16 cinkana anthu omwewo atatu akadakhala m'mwemo, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sakadapulumutsa ana amuna kapena akazi; iwo akadapulumuka okha; koma dziko likadakhala lacipululu.
17 Kapena ndikadza pa dziko ndi lupanga, ndi kuti, Lupanga lipite pakati pa dziko, kuti ndilidulire munthu ndi nyama;