5 Taonani, pokhala wamphumphu sunayenera nchito iri yonse, nanga utanyeketsa moto nupserera udzayeneranso nchito iri yonse?
6 Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Ngati mtengo wampesa pakati pa mitengo ya kunkhalango ndauponya kumoto ukhale nkhuni, momwemo ndidzapereka okhala m'Yerusalemu.
7 Ndipo ndidzaika nkhope yanga iwatsutse; adzaturuka kumoto, koma moto udzawatha; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakuika Ine nkhope yanga iwatsutse.
8 Ndipo ndidzasandutsa dziko cipululu; popeza anacita colakwa, ati Ambuye Yehova.