1 Anandidzeranso mau a Yehova, akuti,
2 Wobadwa ndi munthu iwe, Dziwitsa Yerusalemu zonyansa zace, nuziti,
3 Atero Ambuye Yehova kwa Yerusalemu, Ciyambi cako ndi kubadwa kwako ndiko ku dziko la Akanani; atate wako anali M-amori, ndi mai wako Mhiti.
4 Ndipo za kubadwa kwako, tsiku lobadwa iwe sanadula ncofu yako, sanakuyeretsa ndi kukusambitsa ndi madzi, sanakuthira mcere konse, kapena kukukulunga m'nsaru ai.
5 Panalibe diso linakucitira cifundo, kukucitira cimodzi conse ca izi, kucitira iwe nsoni; koma unatayidwa kuyere; pakuti ananyansidwa nao moyo wako tsiku la kubadwa kwake,
6 Ndipo popita Ine panali iwepo, ndinakuona ulikubvimvinizika m'mwazi wako. Pamenepo ndinanena ndi iwe m'mwazi wako, Khala ndi moyo, inde ndinati kwa iwe m'mwazi mwako, Khala ndi moyo.
7 Ndinakucurukitsa ngati mphundu za kumunda; ndipo unathululuka ndi kukula kufikira wakongola nkhope, maere ako anamera, ndi tsitsi lako linamera; koma unali wamarisece ndi wausiwa.