12 Momwemo ndinaika cipini m'mphuno mwako, ndi maperere m'makutu mwako, ndi korona wokongola pamutu pako.
13 Ndipo unadzikometsera ndi golidi, ndi siliva, ndi cobvala cako ndi bafuta ndi silika ndi yopikapika; unadya ufa wosalala, ndi uci, ndi mafuta; ndipo unali wokongola woposa ndithu, ndipo unapindula-pindula kufikira unasanduka ufumu.
14 Ndi mbiri yako inabuka mwa amitundu cifukwa ca kukongola kwako; pakuti ndiko kwangwiro, mwa ulemerero wanga ndinauika pa iwe, ati Ambuye Yehova.
15 Koma unatama kukongola kwako, ndi kucita zacigololo potama mbiri yako, ndi kutsanulira zigololo zako pa munthu ali yense wopitapo; unali wace.
16 Ndipo unatengako zobvala zako, ndi kudzimangira misanje ya mawanga mawanga, ndi kucitapo cigololo; zotere sizinayenera kufika kapena kucitika.
17 Unatenganso zokometsera zako zokoma za golidi wanga ndi siliva wanga, zimene ndinakupatsa, ndi kudzipangira mafano a amuna, ndi kucita nao cigololo.
18 Unatenganso zobvala zako za nsaru yopikapika, ndi kuwabveka nazo, unaikanso mafuta anga ndi cofukiza canga pamaso pao.