14 Koma ndinacicita cifukwa ca dzina langa, kuti lisaipsidwe pamaso pa amitundu amene ndinawaturutsa pamaso pao.
15 Ndipo ndinawakwezeranso dzanja langa m'cipululu, kusawalowetsa m'dzikolo ndidawapatsa, moyenda mkaka ndi uci, ndilo lokometsetsa mwa maiko onse;
16 popeza ananyoza maweruzo anga, osayenda m'malemba anga, naipsa masabata anga; pakuti mitima yao inatsata mafano ao.
17 Koma diso langa lidawaleka osawaononga, sindinawatha onse m'cipululu.
18 Ndipo ndinati kwa ana ao m'cipululu, Musamayenda m'malemba a atate anu, musawasunga maweruzo ao, kapena kudzidetsa ndi mafano ao;
19 Ine ndine Yehova Mulungu wanu, muziyenda m'malemba anga, ndi kusunga maweruzo anga, ndi kuwacita;
20 muzipatulanso masabata anga, ndipo adzakhala cizindikilo pakati pa Ine ndi inu, kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.