9 Wobadwa ndi munthu iwe, nenera ndi kuti, Atero Yehova, Nena, Lupanga, lupanga lanoledwa, latuulidwanso;
10 lanoledwa kuti liphetu, lituulidwa kuti linge mphezi; tisekererepo kodi? ndilo ndodo yacifumu ya mwana wanga, yopeputsa mtengo uli wonse.
11 Ndipo analipereka alituule, kuti acite nalo lupangali analinola, inde analituula kulipereka m'dzanja la wakupha.
12 Pfuula ndi kulira, wobadwa ndi munthu iwe, pakuti likhalira pa anthu anga, likhalira pa akalonga onse a Israyeli, laperekedwa kulupanga pamodzi ndi anthu anga; cifukwa cace panda pancafu pako.
13 Pakuti pali kuyesedwa; ndipo nanga ndodo yacifumu yopeputsa ikapanda kukhalanso? ati Ambuye Yehova.
14 Ndipo wobadwa ndi munthu iwe, nenera, nuombe manja, lupanga lipitirize katatu, lupanga la wolasidwa ndilo lupanga la wolasidwa wamkuruyo, limene liwazinga.
15 Ndalozetsa nsonga ya lupanga ku zipata zao zonse, kuti mtima wao usungunuke, ndi kukhumudwa kwao kucuruke; ha! analituula linyezimire, analisongoza liphe,