2 Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, udzaweruza, udzauweruza mudziwo wa mwazi kodi? uudziwitse tsono zonyansa zace zonse.
3 Nuziti, Atero Ambuye Yehova, Ndiwo mudzi wokhetsa mwazi pakati pace, kuti nthawi yace ifike, nudzipangire mafano kudzidetsa nao.
4 Waparamula nao mwazi wako, waukhetsa, nudetsedwa nao mafano ako udawapanga, nuyandikizitsa masiku ako, wafikiranso zako zako; cifukwa cace ndakuika ukhale citonzo ca amitundu ndi coseketsa ca maiko onse.
5 Okhala pafupi ndi okhala patali adzakuseka pwepwete, wodetsedwa dzina iwe, wodzala ndi kusokosera.
6 Taona akalonga a Israyeli, yense monga mwa mphamvu yace, akhala mwa iwe, kuti akhetse mwazi.
7 Mwa iwe anapepula atate ndi mai, pakati pa iwe anamcitira mlendo momzunza, mwa iwe anazunza ana amasiye, ndi mkazi wamasiye.
8 Wanyoza zopatulika zanga, waipsa masabata anga.