27 Akalonga ace m'kati mwace akunga afisi akumwetula nyama, kukhetsa mwazi, kuononga miyoyo, kuti aone phindu lonyenga.
28 Ndipo aneneri ao anawamatira ndi dothi losapondeka, ndi kuonera zopanda pace, ndi kuwaombezera mabodza, ndi kuti, Atero Ambuye Yehova posanena Yehova.
29 Anthu a m'dziko anazunzazunza, nalandalanda mwaciwawa, napsinja ozunzika ndi aumphawi, nazunza mlendo wopanda cifukwa.
30 Ndipo ndinafunafuna munthu pakati pao wakumanganso linga, ndi kuimira dziko popasukira pamaso panga, kuti ndisaliononge; koma ndinapeza palibe.
31 Cifukwa cace ndinawatsanulira ukali wanga, ndawatha ndi moto wa kuzaza kwanga, njira yao yao ndinaibweza pa mutu pao, ati Ambuye Yehova.