7 Mwa iwe anapepula atate ndi mai, pakati pa iwe anamcitira mlendo momzunza, mwa iwe anazunza ana amasiye, ndi mkazi wamasiye.
8 Wanyoza zopatulika zanga, waipsa masabata anga.
9 Anthu oneneza anali mwa iwe, kuti akhetse mwazi; ndipo anadya pamapiri mwa iwe, pakati pa iwe anacita zamanyazi.
10 Anabvula umarisece wa atate ao mwa iwe, mwa iwe anacepsa wodetsedwa ndi kooloka kwace.
11 Ndipo wina anacita conyansa ndi mkazi wa mnansi wace, winanso wadetsa mpongozi wace mwamanyazi, ndi wina mwa iwe anaipitsa mlongo wace mwana wamkazi wa atate wace.
12 Analandira mphotho mwa iwe kukhetsa mwazi, walandira phindu loonjezerapo, wanyengerera anansi ako ndi kuwazunza, ndipo wandiiwala Ine, ati Ambuye Yehova.
13 Taona, ndaomba manja pa phindu lako lonyenga waliona, ndi pa mwazi wokhala pakati pako.