10 Iwowa anabvula umarisece wace, anatenga ana ace amuna ndi akazi, namupha iyeyu ndi lupanga; ndi dzina lace linamveka mwa akazi atamcitira maweruzo.
11 Pamene mng'ono wace Oholiba anaciona, anabvunda ndi kuumirira kwace koposa iyeyo; ndi zigololo zace zidaposa zigololo za mkuru wace.
12 Anaumirira Aasuri, ziwanga, ndi akazembe oyandikizana naye, obvala zangwiro, anthu oyenda pa akavalo, onsewo anyamata ofunika.
13 Ndipo ndinamuona kuti anadetsedwa, onse awiri adatenga njira yomweyi.
14 Ndipo anaonjeza zigololo zace, naona amuna olembedwa pakhoma, zithunzithunzi za Akasidi olembedwa ndi kundwe;
15 omangira malamba m'cuuno mwao, ndi nduwira zazikuru zonika pamitu pao, maonekedwe ao ngati akalonga onsewo, akunga a ku Babulo, dziko la kubadwa kwao ndi Kasidi.
16 Ndipo pakuwaona anawalakalaka, nawatumira mithenga ku dziko la Akasidi.