33 Udzadzala ndi kuledzera ndi cisoni, ndi cikho codabwitsa ndi ca cipasuko, ndi cikho ca mkuru wako Samariya.
34 Udzamwa ici ndi kugugudiza, ndi kuceceta-ceceta zibade zace, ndi kung'amba maere ako; pakuti ndacinena, ati Ambuye Yehova.
35 Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Popeza wandiiwala Ine, ndi kunditaya pambuyo pako, uzisenza iwenso coipa cako ndi zigololo zako.
36 Ndipo Yehova anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, kodi udzaweruza Ohola ndi Oholiba? uwafotokozere tsono zonyansa zao.
37 Pakuti anacita cigololo, ndi m'manja mwao muli mwazi, ndipo anacita cigololo ndi mafano ao, nawapititsiranso pamoto ana ao amuna amene anandibalira, kuti athedwe.
38 Anandicitiranso ici, anadetsa malo anga opatulika tsiku lomwelo naipsa masabata anga;
39 pakuti ataphera mafano ao, ana ao analowa tsiku lomwelo m'malo anga opatulika kuwadetsa; ndipo taona, anatero m'kati mwa nyumba yanga.