1 Ndipo kunali caka cakhumi ndi cimodzi, tsiku loyamba la mwezi, anandidzera mau a Yehova, akuti,
2 Wobadwa ndi munthu iwe, popeza Turo ananyodola Yerusalemu, ndi kuti, Onyo, watyoka uwu udali cipata ca mitundu ya anthu; wanditembenukira ine; ndidzakhuta ine, wapasuka uwu;
3 cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Taona ndikutsutsa iwe, Turo, ndidzakukweretsera amitundu, monga nyanja iutsa mafunde ace.
4 Ndipo adzagumula malinga a Turo, ndi kugwetsa nsanja zace; inde ndidzausesa pfumbi lace, ndi kuuyesa pathanthwe poyera.
5 Udzakhala poyanika khokapakati pa nyanja, pakuti Ine ndacinena, ati Ambuye Yehova; ndipo udzakhala cofunkha ca amitundu.
6 Ndi ana ace akazi okhala kumunda adzaphedwa ndi lupanga; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
7 Pakuti atero Ambuye Yehova, Taona ndidzafikitsira Turo Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo, mfumu ya mafumu, yocokera kumpoto ndi akavalo, ndi magareta, ndi apakavalo, ndi msonkhano wa anthu ambiri.