18 Wobadwa ndi munthu iwe, lirira aunyinji a Aigupto, nuwagwetsere iye ndi ana akazi a amitundu omveka kunsi kwa dziko, pamodzi ndi iwo akutsikira kudzenje.
19 Uposa yani m'kukoma kwako? tsika, nuikidwe ndi osadulidwa.
20 Adzagwa pakati pa iwo ophedwa ndi lupanga, operekedwa kwa lupanga, mkokereko ndi aunyinji ace onse.
21 Amphamvu oposa ali m'kati mwa manda adzanena naye, pamodzi ndi othandiza ace, Anatsikira, agonako osadulidwawo, ophedwa ndi lupanga,
22 Asuri ali komwe ndi msonkhano wace wonse, manda ace amzinga; ophedwa onsewo, adagwa ndi lupanga;
23 manda ao aikidwa ku malekezero a dzenje, ndi gulu lace lizinga manda ace; ophedwa onsewo adagwa ndi lupanga, amene anaopsetsa m'dziko la amoyo.
24 Elamu ali komwe ndi gulu lace lonse lozinga manda ace; ophedwa onsewo, adagwa ndi lupanga; amene anatsikira osadulidwa kunsi kwace kwa dziko, amene anaopsetsa m'dziko la amoyo, nasenza manyazi ao, pamodzi ndi iwo akutsikira kudzenje.