13 Ndikanena kwa wolungama kuti adzakhala ndi moyo ndithu, akatama cilungamo cace, akacita cosalungama, sizikumbukika zolungama zace ziri zonse; koma m'cosalungama cace anacicita momwemo adzafa.
14 Ndipo ndikanena kwa woipa, Udzafa ndithu: koma akabwerera iye kuleka cimo lace, nakacita coyenera ndi colungama;
15 woipayo akabweza cikole, nakabweza ico anacilanda mwacifwamba, nakayenda m'malemba a moyo wosacita cosalungama, adzakhala ndi moyo ndithu, sadzafa.
16 Zoipa zace ziri zonse anazicita sizidzakumbukika zimtsutse, anacita coyenera ndi colungama; adzakhala ndi moyo ndithu.
17 Koma ana a anthu a mtundu wako akuti, Njira ya Ambuye siiyenera; koma iwowa njira yao siiyenera.
18 Akabwerera wolungama kuleka cilungamo cace, nakacita cosalungama, adzafa m'mwemo.
19 Ndipo woipa akabwerera kuleka coipa cace, nakacita coyenera ndi colungama, adzakhala ndi moyo nazo.