11 Pakuti atero Ambuye Yehova, Taonani, Ine, Inedi ndidzapwaira nkhosa zanga ndi kuzifunafuna.
12 Monga mbusa afunafuna nkhosa zace tsiku lokhala iye pakati pa nkhosa zace zobalalika, mamwemo ndidzafunafuna nkhosa zanga; ndipo ndidzawalanditsa m'malo monse anabalalikamo tsiku la mitambo ndi la mdima.
13 Ndipo ndidzaziturutsa mwa mitundu ya anthu, ndi kuzisonkhanitsa m'maiko, ndi kulowa nazo m'dziko lao; ndipo ndidzazidyetsa pa mapiri a Israyeli, patimitsinje, ndi ponse pokhala anthu m'dziko.
14 Ndidzazidyetsa podyetsa pabwino; ndi pa mapiri atali a Israyeli padzakhala kholo lao, apo adzagona m'khola mwabwino, nadzadya podyetsa pokometsetsa pa mapiri a Israyeli.
15 Ine ndekha ndidzadyetsa nkhosa zanga, ndi kuzigonetsa, ati Ambuye Yehova.
16 Ndidzafuna yotayika, ndi kubweza yopitikitsidwa, ndi kulukira chika yotyoka mwendo, ndi kulimbitsa yodwalayo; koma yanenepa ndi yolimba ndidzaziononga, ndidzazidyetsa ndi ciweruzo.
17 Ndipo inu, gulu langa, atero Ambuye Yehova, ndiweruza pakati pa zoweta ndi zoweta, nkhosa zamphongo ndi atonde.