1 Ndipo iwe, wobadwa ndi munthu, unenere kwa mapiri a Israyeli, uziti, Mapiri a Israyeli inu, imvani mau a Yehova.
2 Atero Ambuye Yehova, Popeza mdani ananena za inu, Onyo, ingakhale misanje yakale iri yathu, colowa cathu;
3 cifukwa cace unenere, nuti, Atero Ambuye Yehova, Cifukwa, inde cifukwa kuti anakupasulani, nakumemezani pozungulira ponse, kuti mukhale colowa ca amitundu otsala, ndipo mwafika pa milomo ya akazitape, ndi pa mbiri yoipa ya anthu;
4 cifukwa cace, mapiri inu a Israyeli, imvani mau a Ambuye Yehova. Atero Ambuye Yehova kunena ndi mapiri, ndi zitunda, ndi mitsinje, ndi zigwa, ndi zipululu zopasuka, ndi midzi yamabwinja, imene yakhala cakudya ndi coseketsa amitundu otsala akuzungulira;