18 Ndipo ana a anthu amtundu wako akanena ndi iwe, ndi kuti, Sutifotokozera nanga zitani izi?
19 unene nao, Atero Ambuye Yehova, Taonani, ndidzatenga mtengo wa Yosefe uli m'dzanja la Efraimu, ndi wa mafuko a Israyeli anzace, ndi kuwaika pamodzi ndi mtengo wa Yuda, ndi kuiyesa mtengo umodzi; ndipo idzakhala umodzi m'dzanja langa.
20 Ndipo mitengo imene ulembapo idzakhala m'dzanja mwako pamaso pao.
21 Nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Taonani, ndidzatenga ana a Israyeli pakati pa amitundu kumene adamkako, ndi kuwasokolotsa ku mbali zonse, ndi kulowa nao m'dziko mwao;
22 ndipo ndidzawayesa mtundu umodzi m'dzikomo, pa mapiri a Israyeli; ndipo mfumu imodzi idzakhala mfumu ya iwo onse, sadzakhalanso mitundu iwiri, kapena kugawanikanso maufumu awiri konse ai.
23 Ndipo sadzadzidetsanso ndi mafano ao, kapena ndi zonyansa zao, kapena ndi zolakwa zao ziri zonse; koma ndidzawapulumutsa mokhala mwao monse m'mene anacimwamo, ndi kuwayeretsa; m'mwemo adzakhala anthu anga, ndi Ine ndidzakhala Mulungu wao.
24 Ndi mtumiki wanga Davide adzakhala mfumu yao, ndipo iwo onse adzakhala ndi mbusa mmodzi, adzayendanso m'maweruzo anga, nadzasunga malemba anga ndi kuwacita.