4 Udzagwa pa mapiri a Israyeli, iwe ndi magulu ako onse, ndi mitundu ya anthu okhala ndi iwe; ndidzakupereka kwa mbalame zolusa za mitundu yonse, ndi kwa zirombo za kuthengo, akuyese cakudya.
5 Udzagwa kuthengo koyera, pakuti ndanena ndine, ati Ambuye Yehova.
6 Ndipo ndidzatumizira moto Magogi, ndi iwo okhala mosatekeseka m'zisumbu; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
7 Ndipo ndidzadziwikitsa dzina langa loyera pakati pa anthu anga Israyeli, osalola dzina langa loyera aliipsenso; ndipo amitundu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Woyerayo wa Israyeli.
8 Taonani, cikudza, cidzacitika, ati Ambuye Yehova, ndilo tsiku ndanenalo.
9 Ndipo iwo okhala m'midzi ya Israyeli adzaturuka, nadzasonkha moto, nadzatentha zida za nkhondo, ndi zikopa zocinjiriza, mauta, ndi mibvi, ndi ndodo, ndi mikondo; ndipo adzasonkha moto nazo zaka zisanu ndi ziwiri;
10 osatenga nkhuni kuthengo, kapena kuzitema kunkhalango; popeza adzasonkha moto ndi zidazo; nadzafunkha iwo amene anawafunkha, ndi kulanda zao za iwo adalanda zaozo, ati Ambuye Yehova.