1 Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, dzitengere njerwa, nulike pamaso pako, nulembepo mudzi, ndiwo Yerusalemu;
2 nuuzinge, nuumangire nsanja zouzinga, nuundire nthumbira, ndi kuumangira misasa, nuuikire zogumulira pozungulira pace.
3 Nudzitengere ciwaya cacitsulo, ndi kuciika ngati khoma lacitsulo pakati pa iwe ndi mudziwo; nuulozetsere nkhope yako kuti umangidwire misasa, ndipo udzamangira misasa. Ici cikhale cizindikilo ca nyumba ya Israyeli.
4 Ndipo iwe ugonere pansi mbali yako ya kumanzere, nuikepo mphulupulu ya nyumba ya Israyeli; monga mwa kuwerenga kwa masiku amene udzagonapo udzasenza mphulupulu yao.