14 Pamenepo ndinati, Ha, Ambuye Yehova! taonani, moyo wanga sunadetsedwa, pakuti ciyambire ubwana wanga mpaka tsopano sindinadye cinthu cakufa cokha, kapena cogwidwa ndi cirombo; simunalowanso m'kamwa mwanga nyama yonyansa.
15 Ndipo anati kwa ine, Taona ndakuninkha ndowe ya ng'ombe m'malo mwa zonyansa za munthu, uoce mkate wako pamenepo.
16 Nanenanso nane, Wobadwa ndi munthu iwe, taona, ndidzatyola mcirikizo, ndiwo cakudya, m'Yerusalemu; ndipo adzadya cakudyaco monga mwa muyeso, ndi mosamalira, nadzamwa madzi monga mwa muyeso, ndi kudabwa;
17 kuti asowe cakudya ndi madzi, nasumwesumwe, naondetse mu mphulupulu zao.