7 Ndipo ulozetse nkhope yako kuzingidwa kwace kwa Yerusalemu, ndi dzanja lako losapfundika, nuunenere.
8 Ndipo taona ndidzakumanga ndi zingwe zolimba kuti usakunkhulire, mpaka watsiriza masiku a kuzingidwa kwako.
9 Udzitengerenso tirigu, ndi barele, ndi nyemba, ndi mphodza, ndi mapira, ndi mawere, nuziike m'mbale imodzi, ndi kudzipangira mkate nazo; uzidyako monga mwa kuwerenga kwa masiku udzagonawo pambali pako, ndiwo masiku mazana atatu mphambu makumi asanu ndi anai.
10 Ndipo cakudya cako uzicidya ciyesedwe masekeli makumi awiri tsiku limodzi; uzidyako tsiku ndi tsiku pa nthawi yace.
11 Uzimwanso madzi monga mwa muyeso, limodzi la magawo asanu ndi limodzi la hini; uzimwako tsiku ndi tsiku pa nthawi yace.
12 Ndipo uzicidya ngati timikate ta barele, ndi kutioca pamaso pao ndi zonyansa za munthu.
13 Ndipo Yehova anati, Motero ana a Israyeli adz adya ca kudya cao codetsedwa, mwa amitundu kumene ndidzawaingitsirako.