11 Ndi makomo a zipinda za m'mphepete analoza kumpatawo, khomo lina kumpoto, ndi lina kumwela; ndi malo a pa mpatawo anayesa mikono isanu kupingasa kwace pozungulira pace.
12 Ndipo nyumba inali kutsogolo kwa mpata wa mbali ya kumadzulo inali ya mikono makumi asanu ndi awiri kupingasa kwace; ndi khoma la nyumbayo pozungulira pace linali la mikono isanu kucindikira kwace; ndi m'litali mwace mikono makumi asanu ndi anai.
13 Momwemo anayesa kacisi m'litali mwace mikono zana limodzi; ndi mpatawo, ndi nyumbayo, ndi makoma ace, mikono zana limodzi;
14 kupingasa kwace komwe kwa kukhomo kwa nyumba, ndi ku mpatawo kum'mawa, mikono zana limodzi.
15 Momwemo anayesa m'litali mwace nyumbayo inali kutsogolo kwace kwa mpata wokhala cakuno cace, ndi makonde ace am'mwamba, cakuno ndi cauko, mikono zana limodzi, ndi Kacisi wa m'katimo, ndi makonde a kubwalo;
16 ziundo, ndi mazenera a made okhazikika, ndi makonde am'mwamba akuzinga zipinda zosanjikizana zao zitatu, pandunji pa ciundo, ocinga ndi matabwa pozungulira pace, kuyambira pansi kufikira kumazenera; koma mazenera anaphimbika;
17 kufikira pamwamba pa khomo, mpaka nyumba ya m'katimo, ndi kunja kwace, ndi khoma lonse kwete m'kati ndi kunja, monga mwa miyeso.