7 Ndipo zipinda za m'mphepete zinakula m'kupingasa kwao, pozinga nyumba m'kukwera kwao; pakuti nyumba inazingika mokwerakwera pozungulira pace pa nyumba; motero kupingasa kwace kwa nyumba kunakula kumwamba kwace, momwemonso anakwera kuyambira cipinda cakunsi, kupita capakati, kufikira cam'mwamba.
8 Ndinaonanso kuti kunyumba kunali ciunda pozungulira pace; maziko a zipinda za m'mphepete anafikira muyeso wa bango la mikono isanu ndi umodzi yaikuru.
9 Kucindikira kwa khoma la kuzipinda za m'mphepete kunja kwace kunali mikono isanu; ndipo mpata wace unali malo olowera m'zipinda za m'mphepete za kacisi.
10 Ndi pakati pa zipinda panali kupingasa kwa mikono makumi awiri, pozungulira pace ponse pa nyumba.
11 Ndi makomo a zipinda za m'mphepete analoza kumpatawo, khomo lina kumpoto, ndi lina kumwela; ndi malo a pa mpatawo anayesa mikono isanu kupingasa kwace pozungulira pace.
12 Ndipo nyumba inali kutsogolo kwa mpata wa mbali ya kumadzulo inali ya mikono makumi asanu ndi awiri kupingasa kwace; ndi khoma la nyumbayo pozungulira pace linali la mikono isanu kucindikira kwace; ndi m'litali mwace mikono makumi asanu ndi anai.
13 Momwemo anayesa kacisi m'litali mwace mikono zana limodzi; ndi mpatawo, ndi nyumbayo, ndi makoma ace, mikono zana limodzi;