1 Pamenepo anamuka nane ku cipata coloza kum'mawa,
2 ndipo taonani, ulemerero wa Mulungu wa Israyeli unadzera njira ya kum'mawa, ndi mau ace ananga mkokomo wa madzi ambiri, ndi dziko linanyezimira ndi ulemerero wace.
3 Ndipo maonekedwe a masomphenya ndinawaona anali monga masomphenya aja ndinawaona pakudza ine kupasula mudzi; ndi masomphenyawa anali ngati masomphenya aja ndinawaona ku mtsinje wa Kebara; ndipo ndinagwa nkhope pansi.
4 Ndipo ulemerero wa Yehova unalowa m'kacisi kudzera njira ya cipata coloza kum'mawa.
5 Ndipo mzimu unandinyamula numuka nane ku bwalo la m'kati; ndipo taonani, ulemerero wa Mulungu unadzaza kacisi.
6 Ndipo ndinamva wina alikulankhula nane ali m'kacisi, naima nane munthu.
7 Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, pano mpokhala mpando wacifumu wanga, mpoponda ku mapazi anga, pomwe ndidzakhala pakati pa ana a Israyeli kosatha; ndi nyumba ya Israyeli siidzadetsanso dzina langa loyera, ngakhale iwo kapena mafumu ao, mwa cigololo cao, ndi mitembo ya mafumu ao pa misanje yao,