2 Ndipo Yehova anati kwa ine, Cipata ici citsekeke, cisatseguke, osalowako munthu; pakuti Yehova Mulungu wa Israyeli walowerapo; cifukwa cace citsekeke.
3 Koma kunena za kalonga, iye akhale m'menemo monga kalonga kudya mkate pamaso pa Yehova; alowe ku njira ya ku khonde la cipata, naturukire njira yomweyi.
4 Atatero anamuka nane njira ya cipata ca kumpoto kukhomo kwa kacisi, ndipo ndinapenya, taonani, ulemerero wa Yehova unadzaza nyumba ya Yehova; pamenepo ndinagwa nkhope pansi.
5 Ndipo Yehova anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, samalira bwino, nupenye ndi maso ako, numve m'makutu mwako zonse ndidzanena nawe, kunena za malemba onse a nyumba ya Yehova, ndi malamulo ace onse; nusamalire bwino malowedwe a nyumbayi, ndi maturukidwe ace onse a malo opatulika.
6 Nunene kwa opandukawo, kwa nyumba ya Israyeli, Atero Ambuye Yehova, Nyumba ya Israyeli inu, Zikukoleni zonyansa zanu zonse;
7 popeza mwalowa nao acilendo osadulidwa m'mtima, osadulidwa m'thupi akhale m'malo anga opatulika kuwadetsa, ndiwo nyumba yanga, popereka inu mkate wanga, mafuta, ndi mwazi; ndipo munatyola pangano langa pamodzi ndi zonyansa zanu zonse.
8 Ndipo simunasunga udikiro wa zopatulika zanga, koma mwadziikira mokha osunga udikiro wanga m'malo anga opatulika.