7 Ndipo kalonga adzakhala nalo gawo lace mbali yina ndi mbali inzace ya cipereko copatulika, ndi ya dziko la mudzi, kutsogolo kwa cipereko copatulika, ndi kutsogolo kwa dziko la mudzi, mbali ya kumadzulo kumadzulo, ndi mbali ya kum'mawa kum'mawa; ndi m'litali mwace mudzalingana ndi limodzi la magawo, kuyambira ku malire a kumadzulo kufikira malire a kum'mawa.
8 M'dzikomo ili lidzakhala lace lace m'Israyeli; ndipo akalonga anga sadzazunzanso anthu anga, koma adzapereka dziko kwa nyumba ya Israyeli monga mwa mapfuko ao.
9 Atero Ambuye Yehova, Likufikireni akalonga a Israyeli inu, lekani kucita ciwawa, ndi kulanda za eni ace; mucite ciweruzo ndi cilungamo; lekani kupitikitsa anthu anga m'zolowa zao, ati Ambuye Yehova.
10 Muzikhala nayo miyeso yoona, ndi efa woona, ndi bati loona.
11 Efa ndi bati zikhale za muyeso umodzi, bati liyese limodzi la magawo khumi la homeri, efa lomwe liyese limodzi la magawo khumi la homeri; muyeso wao uyesedwa monga mwa homeri.
12 Ndipo sekeli ndilo magera makumi awiri; masekeli makumi awiri, ndi masekeli awiri ndi asanu, ndi masekeli khumi ndi asanu, ndiwo mane wanu.
13 Copereka mucipereke ndico limodzi la magawo asanu ndi limodzi la efa, kulitapa pa homeri wa tirigu; muperekenso limodzi la magawo asanu ndi limodzi la efa, kulitapa pa homeri wa barele;