1 Ndipo anandibwezera ku khomo la nyumba, ndipo taonani, panatumphuka madzi pansi pa ciundo ca nyumba kum'mawa; pakuti khomo lace la nyumba linaloza kum'mawa; ndipo madzi anatsika kucokera pansi pa nyumba, ku mbali ya lamanja lace, kumwela kwa guwa la nsembe.
2 Pamenepo anaturuka nane njira ya ku cipata ca kumpoto, nazungulira nane njira yakunja kumka ku cipata cakunja, njira ya ku cipata coloza kum'mawa; ndipo taonani, panaturuka madzi pa mbali ya kulamanja.
3 Poturuka munthuyu kumka kum'mawa ndi cingwe coyesera m'dzanja lace, anayesa mikono cikwi cimodzi, nandipititsa pamadzi, madzi oyesa m'kakolo.
4 Nayesanso cikwi cimodzi, nandipititsa pamadzi, madzi oyesa m'maondo. Nayesanso cikwi cimodzi, nandipititsa pamadzi, madzi oyesa m'cuuno.
5 Atatero anayesanso cikwi cimodzi, ndipo mtsinje wosakhoza kuoloka ine, popeza madzi adakula, madzi osambira, mtsinje wosaoloka munthu.