4 Nutengekonso pa amenewa ndi kuwaponya pakati pa moto, ndi kuwatentha m'moto; kucokera kumeneko udzaturuka moto pa nyumba yonse ya Israyeli.
5 Atero Yehova Mulungu, Uwu ndi Yerusalemu ndinauika pakati pa amitundu, ndi pozungulira pace pali maiko.
6 Koma anakaniza maweruzo anga ndi kucita zoipa koposa amitundu, nakaniza malemba anga koposa maiko akuuzungulira; pakuti anataya maweruzo anga, ndi malemba anga, sanayendamo.
7 Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Popeza kupokosera kwanu kwaposa kwa amitundu akukuzingani, ndipo simunayenda m'malemba anga, kapena kucita maweruzo anga, ngakhale maweruzo a amitundu akukuzingani simunawacita;
8 cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Taona ndidzatsutsana nawe Inedi, ndi kucita maweruzo pakati pako pamaso pa amitundu.
9 Ndipo ndidzacita mwa iwe cimene sindinacicita ndi kale lonse, ndi kusadzacitanso momwemo, cifukwa ca zonyansa zako zonse.
10 Cifukwa cace atate adzadya ana pakati pako, ndi ana adzadya atate ao; ndipo ndidzacita maweruzo mwa iwe, ndi akutsala onse ndidzawabalalitsa ku mphepo zonse.