11 Ciwawa cauka cikhale ndodo ya coipa; sadzawatsalira ndi mmodzi yense, kapena wa unyinji wao, kapena wa cuma cao; sipadzakhalanso kuwalira maliro.
12 Yafika nthawi, layandikira tsikulo, wogula asakondwere, ndi wogulitsa asamve cisoni; pakuti mkwiyo ukhalira unyinji wao wense.
13 Pakuti wogulitsa sadzabwera ku cogulitsaco, cinkana akali ndi moyo, popeza masomphenyawo akunena unyinji wace wonse sadzapita pacabe, ndipo palibe mmodzi adzalimbitsa moyo wace m'mphulupulu yace.
14 Aomba lipenga, nakonzeratu zonse, koma palibe womuka kunkhondo; pakuti mkwiyo wanga ukhalira unyinji wace wonse.
15 Kunja kuli lupanga, ndi m'katimo muli mliri ndi njala; wokhala kuthenso adzafa ndi lupanga, ndi wokhala m'mudziyo njala ndi mliri zidzamutha.
16 Ndipo akupulumuka mwa iwo adzapulumuka, koma adzakhala kumapiri ngati njiwa za kuzigwa, onse akubuula, ali yense m'mphulupulu zace.
17 Manja onse adzalenda, ndi maondo onse adzaweyeseka ngati madzi.