1 Pamenepo Iye anapfuula m'makutu mwanga ndi mau akuru, ndi kuti, Asendere oyang'anira mudzi, ali yense ndi cida cace coonongera m'dzanja lace.
2 Ndipo taonani, anadza amuna asanu ndi mmodzi, odzera njira ya cipata ca kumtunda coloza kumpoto, ali yense ndi cida cace cophera m'dzanja lace; ndi munthu mmodzi pakati pao wobvala bafuta, ndi zolembera nazo m'cuuno mwace. Ndipo analowa, naima m'mphepete mwa guwa la nsembe lamkuwa.
3 Ndipo ulemerero wa Mulungu wa Israyeli unakwera kucoka pakerubi, pamene unakhalira kumka ku ciunda ca nyumba, naitana munthu wobvala bafutayo wokhala ndi zolembera nazo m'cuuno mwace.
4 Ndipo Yehova ananena naye, Pita pakati pa mudzi, pakati pa Yerusalemu, nulembe cizindikilo pa mphumi zao za anthu akuusa moyo ndi kulira cifukwa ca zonyansa zonse zicitidwa pakati pace.
5 Nati kwa enawo, nditikumva ine, Pitani pakati pa mudzi kumtsata iye, ndi kukantha; maso anu asalekerere, musacite cifundo;