1 Pamene Rakele anaona kuti sanambalira Yakobo ana, Rakele anamcitira mkuru wace nsanje; nati kwa Yakobo, Ndipatse ana ndingafe.
2 Ndipo Yakobo anapsa mtima ndi Rakele; nati, Kodi ine ndikhala m'malo a Mulungu amene akukaniza iwe zipatso za mimba?
3 Ndipo Rakele anati, Taonani mdzakazi wanga Biliha, mulowe kwa iye; ndipo iye adzabala pa maondo anga, kuti inenso ndionerepo ana pa iye.
4 Ndipo Rakele anampatsa iye Biliha mdzakazi wace akhale mkazi wace; ndipo Yakobo analowa kwa iye.
5 Ndipo Biliha anatenga pakati, nambalira Yakobo mwana wamwamuna.
6 Rakele ndipo anati, Mulungu wandiweruzira ine, namva mau anga, nandipatsa ine mwana; cifukwa cace anamucha dzina lace Dani.
7 Ndipo Biliha mdzakazi wace wa Rakele anatenganso pakati, nambalira Yakobo mwana wamwamuna waciwiri.