23 Ndipo anawatenga iwo nawaolotsa pamtsinje, naziolotsa zonseanalinazo.
24 Ndipo anatsala Yakobo yekha; ndipo analimbana naye munthu kufikira mbandakuca.
25 Ndipo pamene anaona kuti sanamlaka, anakhudza nsukunyu ya ncafu yace; ndipo nsukunyu ya ncafu yace ya Yakobo inaguluka, pakulimbana naye.
26 Ndipo iye anati Ndileke ndimuke, cifukwa kulinkuca. Ndipo Yakobo anati, Sindidzakuleka iwe kuti umuke, ukapanda kundidalitsa ine.
27 Ndipo iye anati kwa Yakobo, Dzina lako ndani? Nati iye, Yakobo.
28 Ndipo anati, Dzina lako silidzachedwanso Yakobo, koma Israyeli, cifukwa unayesana naye Mulungu ndithu, ndipo unapambana.
29 Yakobo ndipo anafunsa iye, nati, Undiuze ine dzina lako. Ndipo iye anati, Undifunsa dzina cifukwa ninji? Ndipo anamdalitsa iye pamenepo.