10 Ndipo mudzakhala m'dziko la Goseni, mudzakhala pafupi ndi ine, inu ndi ana anu, ndi ana a ana anu, ndi nkhosa zanu, ndi zoweta zanu, ndi zonse muli nazo;
11 ndipo ndidzacereza inu komweko; pakuti zatsala zaka zisanu za njala; kuti mungafikire umphawi, inu ndi banja lanu, ndi onse muli nao.
12 Taonani, maso anu aona, ndi maso a mphwanga Benjamini, kuti ndi m'kamwa mwanga ndirikulankhula ndi inu.
13 Ndipo mudzafotokozera atate wanga za ulemerero wanga wonse m'Aigupto, ndi zonse mwaziona; ndipo muzifulumira ndi kutsitsira kuno atate wanga.
14 Ndipo anagwa pakhosi pace pa Benjamini, nalira; ndipo Benjamini nalira pakhosi pace.
15 Ndipo anampsompsona abale ace onse, nalilira iwo; ndipo pambuyo pace abale ace onse anaceza naye.
16 Ndipo mbiri yace inamveka m'nyumba ya Farao, kuti abale ace a Yosefe afika; ndipo inamkomera Farao, ndi anyamata ace.