4 Ndipo Yosefe anati kwa abale ace, Muyandikiretu kwa ine; nayandikira. Ndipo iye anati, Ine ndine Yosefe mbale wanu, ine ndemwe munandigulitsa ndilowe m'Aigupto.
5 Tsopano musaphwetekwe mtima, musadzikwiyira inu nokha, kuti munandigulitsira ine kuno, pakuti Mulungu ananditumiza ine patsogolo panu kuti ndisunge moyo.
6 Zaka ziwirizi muli njala m'dziko muno; ndipo zatsala zaka zisanu, zopanda kulima kapena kusenga,
7 Ndipo Mulungu anatumiza ine patsogolo panu kuti ndikhazike inu mutsale m'dziko lapansi, ndi kusunga inu amoyo ndi cipulumutso cacikuru.
8 Ndipo tsopano sindinu amene munanditumiza ine ndifike kuno, koma Mulungu, ndipo anandiyesa ine atate wa Farao, ndi mwini banja lace lonse, ndi wolamulira dziko lonse la Aigupto.
9 Fulumirani, kwerani kunka kwa atate wanga, muti kwa iye, Cotere ati Yosefe mwana wanu, Mulungu wandiyesa ine mwini Aigupto lonse: tsikirani kwa ine, musacedwe.
10 Ndipo mudzakhala m'dziko la Goseni, mudzakhala pafupi ndi ine, inu ndi ana anu, ndi ana a ana anu, ndi nkhosa zanu, ndi zoweta zanu, ndi zonse muli nazo;