15 Ndipo pakupenyerera ine zamoyozo, taonani, njinga imodzi imodzi yoponda pansi pafupi ndi zamoyozo pa nkhope zao zinai.
16 Maonekedwe a njingazi ndi mapangidwe ao ananga mawalidwe a berulo; ndi izi zinai zinafanana mafaniziro ao; ndi maonekedwe ao ndi mapangidwe ao anali ngati njinga ziwiri zopingasitsana.
17 Poyenda zinayenda ku mbali zao zinai, zosatembenuka poyenda.
18 Ndi mikombero yace inali yokuzika ndi yoopsa; ndi izi zinai zinali ndi mikombero yao yodzala ndi maso pozungulira pao.
19 Ndipo poyenda zamoyozo, njingazi zinayenda pambali pao; ndipo ponyamuka pansi zamoyozo, njinga zinanyamuka.
20 Kuli konse mzimu ukuti umuke, zinamuka komwe mzimu ukuti umuke; ndi njingazi zinanyamuka pambali pa izo; pakuti mzimu wa zamoyozo unali m'njingazo.
21 Poyenda zija zinayenda izi, poima zija zinaima izi; ndipo ponyamuka pansi zija njingazi zinanyamuka pambali pa izo; pakuti mzimu wa zamoyozo unali mu njingazi.